|
| 1 |
|
| Mkazi yense wanzeru amanga banja lace; Koma wopusa alipasula ndi manja ace. |
|
| 2 |
|
| Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; Koma wokhota m'njira yace amnyoza, |
|
| 3 |
|
| M'kamwa mwa citsiru muli ntyole ya kudzikuza; Koma milomo ya anzeru Idzawasunga. |
|
| 4 |
|
| Popanda zoweta modyera muti see; Koma mphamvu ya ng'ombe icurukitsa phindu. |
|
| 5 |
|
| Mboni yokhulupirika sidzanama; Koma mboni yonyenga imalankhula zonama. |
|
| 6 |
|
| Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; Koma wozindikira saona bvuto m'kuphunzira. |
|
| 7 |
|
| Pita pamaso pa munthu wopusa, Sudzazindikira milomo yakudziwa. |
|
| 8 |
|
| Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace; Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo. |
|
| 9 |
|
| Zitsiru zinyoza kuparamula; Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano. |
|
| 10 |
|
| Mtima udziwa kuwawa kwace kwace; Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace. |
|
| 11 |
|
| Nyumba ya oipa idzapasuka; Koma hema wa oongoka mtima adzakula. |
|
| 12 |
|
| Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa. |
|
| 13 |
|
| Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni. |
|
| 14 |
|
| Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira zace; Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha. |
|
| 15 |
|
| Wacibwana akhulupirira mau onse; Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace. |
|
| 16 |
|
| Wanzeru amaopa nasiya zoipa; Koma wopusa amanyada osatekeseka. |
|
| 17 |
|
| Wokangaza kukwiya adzacita utsiru; Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa. |
|
| 18 |
|
| Acibwana amalandira colowa ca utsiru; Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona. |
|
| 19 |
|
| Oipa amagwadira abwino, Ndi ocimwa pa makomo a olungama. |
|
| 20 |
|
| Waumphawi adedwa ndi anzace omwe; Koma akukonda wolemera acuruka. |
|
| 21 |
|
| Wonyoza anzace acimwa; Koma wocitira osauka cifundo adala. |
|
| 22 |
|
| Kodi oganizira zoipa sasocera? Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi. |
|
| 23 |
|
| M'nchito zonse muli phindu; Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi. |
|
| 24 |
|
| Korona wa anzeru ndi cuma cao; Utsiru wa opusa ndiwo utsiru. |
|
| 25 |
|
| Mboni yoona imalanditsa miyoyo; Koma wolankhula zonama angonyenga. |
|
| 26 |
|
| Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo. |
|
| 27 |
|
| Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, Kupatutsa ku misampha ya imfa. |
|
| 28 |
|
| Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; Koma popanda anthu kalonga aonongeka. |
|
| 29 |
|
| Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; Koma wansontho akuza utsiru. |
|
| 30 |
|
| Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; Koma nsanje ibvunditsa mafupa. |
|
| 31 |
|
| Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace; Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza. |
|
| 32 |
|
| Wocimwa adzakankhidwa m'kuipa kwace; Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira, |
|
| 33 |
|
| Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira, Nidziwika pakati pa opusa. |
|
| 34 |
|
| Cilungamo cikuza mtundu wa anthu; Koma cimo licititsa pfuko manyazi. |
|
| 35 |
|
| Mfumu ikomera mtima kapolo wocita mwanzeru; Koma idzakwiyira wocititsa manyazi. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | | 34 | | 35 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/proverbs/014.mp3
31
14