|
| 1 |
|
| Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo. |
|
| 2 |
|
| Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru. |
|
| 3 |
|
| Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino. |
|
| 4 |
|
| Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo. |
|
| 5 |
|
| Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera. |
|
| 6 |
|
| M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri; koma m'phindu la woipa muli vuto. |
|
| 7 |
|
| Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama. |
|
| 8 |
|
| Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa. |
|
| 9 |
|
| Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo. |
|
| 10 |
|
| Wosiya njira adzalangidwa mowawa; wakuda chidzudzulo adzafa. |
|
| 11 |
|
| Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu? |
|
| 12 |
|
| Wonyoza sakonda kudzudzulidwa, samapita kwa anzeru. |
|
| 13 |
|
| Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima. |
|
| 14 |
|
| Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa; koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru. |
|
| 15 |
|
| Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha. |
|
| 16 |
|
| Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso. |
|
| 17 |
|
| Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng'ombe yonenepa pali udani. |
|
| 18 |
|
| Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano. |
|
| 19 |
|
| Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga, koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu. |
|
| 20 |
|
| Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake. |
|
| 21 |
|
| Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake. |
|
| 22 |
|
| Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika. |
|
| 23 |
|
| Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake; ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino? |
|
| 24 |
|
| Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda. |
|
| 25 |
|
| Yehova adzapasula nyumba ya wonyada; koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake. |
|
| 26 |
|
| Ziwembu zoipa zinyansa Yehova; koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa. |
|
| 27 |
|
| Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo. |
|
| 28 |
|
| Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa. |
|
| 29 |
|
| Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera. |
|
| 30 |
|
| Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima; ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi. |
|
| 31 |
|
| Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo lidzakhalabe mwa anzeru. |
|
| 32 |
|
| Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru. |
|
| 33 |
|
| Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu. |
|
|
|
|