|
| 1 |
|
| Zolinga zamumtima ndi za munthu, koma zolankhula zake ndi zochokera kwa Chauta. |
|
| 2 |
|
| Ntchito zake za munthu zimakhala zolungama pamaso pake, koma Chauta amaweruza zamumtima. |
|
| 3 |
|
| Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi. |
|
| 4 |
|
| Chauta adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale ndi cholinga chake, ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto. |
|
| 5 |
|
| Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta, ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa. |
|
| 6 |
|
| Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa. |
|
| 7 |
|
| Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere. |
|
| 8 |
|
| Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo. |
|
| 9 |
|
| Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo. |
|
| 10 |
|
| M'kamwa mwa mfumu mumatuluka chigamulo chochokera kwa Mulungu. Pakamwa pa mfumu sipalakwa pogamula mlandu. |
|
| 11 |
|
| Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta. |
|
| 12 |
|
| Kuchita zoipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wao. |
|
| 13 |
|
| Mau oona amakondweretsa mfumu, ndipo imamkonda munthu wolankhula chilungamo. |
|
| 14 |
|
| Mfumu ikakwiya, ndiye kuti imfa ili pafupi, koma munthu wanzeru amaupepesa mkwiyowo. |
|
| 15 |
|
| Kukoma mtima kwa mfumu kumadzetsa moyo, kuli ngati mitambo ya mvula yam'chilimwe. |
|
| 16 |
|
| Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva. |
|
| 17 |
|
| Mseu wa munthu wolungama umapewa zoipa. Munthu wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake. |
|
| 18 |
|
| Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa. |
|
| 19 |
|
| Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada. |
|
| 20 |
|
| Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta. |
|
| 21 |
|
| Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu, kulankhula kwake kokometsera kumakulitsa mphamvu ya mau ake. |
|
| 22 |
|
| Nzeru ndi kasupe wopatsa moyo kwa amene ali nazo, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa anthu opusa. |
|
| 23 |
|
| Mtima wa munthu wanzeru umamlankhulitsa mau ochenjera, nzeruzo zimakulitsa mphamvu ya mau ake. |
|
| 24 |
|
| Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi. |
|
| 25 |
|
| Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa. |
|
| 26 |
|
| Njala ya munthu wantchito imamthandiza kulimbikira, ndi njalayo imene imamkakamiza kuchita kanthu. |
|
| 27 |
|
| Munthu wopandapake amakonzekera kuchita zoipa, mau ake ali ngati moto wopsereza. |
|
| 28 |
|
| Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi. |
|
| 29 |
|
| Munthu wandeu amakopa mnzake, ndipo amamuyendetsa m'njira yoipa. |
|
| 30 |
|
| Amene amatsinzinira masoŵa, amalingalira zinthu zokhota, amene amachita msunamo amadzetsa zoipa. |
|
| 31 |
|
| Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali. |
|
| 32 |
|
| Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda. |
|
| 33 |
|
| Maere amaŵaponya m'funkha, koma amene amaulula ndi Chauta. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/016.mp3
31
16