|
| 1 |
|
| Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona. |
|
| 2 |
|
| Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu. Koma chimangolankhula za maganizo ake okha. |
|
| 3 |
|
| Kuipa mtima kukaoneka, pamabweranso manyozo, kunyozeka kumaitana manyazi. |
|
| 4 |
|
| Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga. |
|
| 5 |
|
| Si kwabwino pa mlandu kukondera munthu woipa, kapena kupondereza munthu wosalakwa. |
|
| 6 |
|
| Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo. |
|
| 7 |
|
| Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo. |
|
| 8 |
|
| Mau a kazitape ali ngati chakudya chokoma, anthu amaŵameza onse mokondwa. |
|
| 9 |
|
| Wogwira ntchito yake mwaulesi, ali pachibale ndi munthu woononga zinthu. |
|
| 10 |
|
| Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka. |
|
| 11 |
|
| Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali limene amayesa ndi lomutchinjiriza. |
|
| 12 |
|
| Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa. |
|
| 13 |
|
| Ukayankha usanamve nkhani yonse, umaoneka wopusa ndipo umachita manyazi. |
|
| 14 |
|
| Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso? |
|
| 15 |
|
| Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu. |
|
| 16 |
|
| Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi, imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu. |
|
| 17 |
|
| Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wokhoza ndiye, mpaka mnzake atabwera nadzamufunsitsa bwino. |
|
| 18 |
|
| Maere amathetsa mikangano. Amalekanitsa okangana amphamvu. |
|
| 19 |
|
| Mnzako ukamthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumakutsekera thandizo lililonse. |
|
| 20 |
|
| Munthu amapeza bwino kapena ai, malinga ndi zolankhula zake, amalandira zotsatira za mau a pakamwa pake. |
|
| 21 |
|
| Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka. |
|
| 22 |
|
| Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino, Chauta wamukomera mtima. |
|
| 23 |
|
| Anthu osauka amapemba, koma anthu olemera amayankha mwaukali. |
|
| 24 |
|
| Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/018.mp3
31
18