|
| 1 |
|
| Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako, |
|
| 2 |
|
| ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu; |
|
| 3 |
|
| ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu, |
|
| 4 |
|
| ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika, |
|
| 5 |
|
| ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova. |
|
| 6 |
|
| Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu. |
|
| 7 |
|
| Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro, |
|
| 8 |
|
| pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama. Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika. |
|
| 9 |
|
| Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo, kusakondera ndi njira iliyonse yabwino. |
|
| 10 |
|
| Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako, kudziwa zinthu kudzakusangalatsa. |
|
| 11 |
|
| Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga; kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza. |
|
| 12 |
|
| Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa, kwa anthu amabodza, |
|
| 13 |
|
| amene amasiya njira zolungama namayenda mʼnjira zamdima, |
|
| 14 |
|
| amene amakondwera pochita zoyipa namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa. |
|
| 15 |
|
| Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota, ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo. |
|
| 16 |
|
| Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika, |
|
| 17 |
|
| amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake. |
|
| 18 |
|
| Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa; njira zake zimamufikitsa ku manda. |
|
| 19 |
|
| Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera kapena kupezanso njira zamoyo. |
|
| 20 |
|
| Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino, uzitsata njira za anthu ochita chilungamo. |
|
| 21 |
|
| Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo; |
|
| 22 |
|
| Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo, ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/002.mp3
31
2