Buku Loyera
|
| 1 |
| Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uyang'ane bwino zimene zili pamaso pako. |
| 2 |
| Ngati ndiwe munthu wadyera, udziletse kuti usachite khwinthi. |
| 3 |
| Usasirire zakudya zake zokoma, poti zimenezi ndi zakudya zonyenga. |
| 4 |
| Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa. |
| 5 |
| Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga. |
| 6 |
| Usadye chakudya kwa munthu waunkhambo, usamalakalaka zakudya zake zokoma. |
| 7 |
| Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu. Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!” Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna. |
| 8 |
| Udzasanza nthongo wadyazo, ndipo mau ako oshashalika adzapita pachabe. |
| 9 |
| Usamalankhula pali munthu wopusa, pakuti adzanyoza mau ako anzeru. |
| 10 |
| Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye. |
| 11 |
| Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo. |
| 12 |
| Mtima wako ukhale pa malangizo, ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru. |
| 13 |
| Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa. |
| 14 |
| Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa. |
| 15 |
| Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. |
| 16 |
| Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama. |
| 17 |
| Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa, koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku. |
| 18 |
| Ndithu, zakutsogolo zilipo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. |
| 19 |
| Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uuyendetse m'njira yabwino. |
| 20 |
| Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera. |
| 21 |
| Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza. |
| 22 |
| Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba. |
| 23 |
| Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu. |
| 24 |
| Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye. |
| 25 |
| Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe. |
| 26 |
| Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine, maso ako apenyetsetse njira zanga. |
| 27 |
| Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza. |
| 28 |
| Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika. |
| 29 |
| Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula? Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake? Ndani ali wofiira maso? |
| 30 |
| Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina. |
| 31 |
| Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero. |
| 32 |
| Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri. |
| 33 |
| Maso ako adzaona zinthu zachilendo, maganizo ndi mau ako adzakhala okhotakhota. |
| 34 |
| Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalaŵa. |
| 35 |
| Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke. Adandimenya, koma ine osamvako. Kodi ine ndidzatsitsimuka liti? Ndiye ndithamangira chakumwa china.” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/023.mp3
31
23