Buku Loyera
|
| 1 |
| Usamachitira nsanje anthu ochimwa, kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo, |
| 2 |
| chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto. |
| 3 |
| Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. |
| 4 |
| Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali. |
| 5 |
| Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu. |
| 6 |
| Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo. |
| 7 |
| Nzeru ndi yapatali kwambiri kwa munthu wopusa, alibe chonena pa bwalo lamilandu. |
| 8 |
| Amene amakonzekera kuchita choipa, adzatchedwa mvundulamadzi. |
| 9 |
| Kukonzekera zopusa nkuchimwa, munthu wonyoza amanyansa anthu. |
| 10 |
| Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa. |
| 11 |
| Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha. |
| 12 |
| Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake? |
| 13 |
| Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino, madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa. |
| 14 |
| Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. |
| 15 |
| Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba ngati munthu woipa mtima, usachite nayo nkhondo nyumba yake. |
| 16 |
| Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse. |
| 17 |
| Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. |
| 18 |
| Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo. |
| 19 |
| Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. |
| 20 |
| Pajatu munthu woipa zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo, moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale. |
| 21 |
| Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu, usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano. |
| 22 |
| Ameneŵa amatha kugwetsa tsoka mwadzidzidzi, ndani angadziŵe kuwopsa kwa chiwonongeko chochokera kwa aŵiriŵa? |
| 23 |
| Enanso ndi aŵa malangizo a anthu anzeru: Kukondera pozenga milandu si chinthu chabwino. |
| 24 |
| Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye. |
| 25 |
| Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri. |
| 26 |
| Munthu woyankha zoona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni. |
| 27 |
| Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba. |
| 28 |
| Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, pakamwa pako pasamanena zonama. |
| 29 |
| Usamanena kuti, “Ndidzamchitira monga momwe iye wandichitira ine, ndidzamlipsira chifukwa cha zomwe iye wandichitira ine.” |
| 30 |
| Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. |
| 31 |
| M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. |
| 32 |
| Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: |
| 33 |
| Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” |
| 34 |
| umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/024.mp3
31
24