|
| 1 |
|
| Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba. |
|
| 2 |
|
| Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu. |
|
| 3 |
|
| Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya, koma mitima ya mafumu singasanthulike. |
|
| 4 |
|
| Chotsera siliva mphala yake, mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale. |
|
| 5 |
|
| Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo. |
|
| 6 |
|
| Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu. |
|
| 7 |
|
| Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona. |
|
| 8 |
|
| Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi. |
|
| 9 |
|
| Nena mlandu wako ndi mnzako, osawulula zinsinsi za mwini; |
|
| 10 |
|
| kuti wakumva angakutonze, mbiri yako yoipa ndi kusachoka. |
|
| 11 |
|
| Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva. |
|
| 12 |
|
| Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera. |
|
| 13 |
|
| Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake. |
|
| 14 |
|
| Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga. |
|
| 15 |
|
| Chipiriro chipembedza mkulu; lilime lofatsa lithyola fupa. |
|
| 16 |
|
| Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze. |
|
| 17 |
|
| Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzikamodzi; kuti angatope nawe ndi kukuda. |
|
| 18 |
|
| Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa. |
|
| 19 |
|
| Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka. |
|
| 20 |
|
| Monga wovula malaya tsiku lamphepo, ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni. |
|
| 21 |
|
| Mdani wako akamva njala umdyetse, akamva ludzu ummwetse madzi. |
|
| 22 |
|
| Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pake; ndipo Yehova adzakupatsa mphotho. |
|
| 23 |
|
| Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope. |
|
| 24 |
|
| Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola. |
|
| 25 |
|
| Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali. |
|
| 26 |
|
| Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa. |
|
| 27 |
|
| Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino; chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu. |
|
| 28 |
|
| Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga. |
|
|
|
|