Buku Loyera
|
| 1 |
| Ulemu woulandira chitsiru uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe, kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola. |
| 2 |
| Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha. |
| 3 |
| Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ncha m'kamwa mwa bulu, chonchonso ndodo ndi yoyenerera zitsiru. |
| 4 |
| Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho. |
| 5 |
| Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru. |
| 6 |
| Amene amatuma chitsiru kukanena uthenga, amachita ngati kudzidula mapazi ndipo amadziitanira mavuto. |
| 7 |
| Monga miyendo ya munthu wopunduka imakhala yopanda ntchito, ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru. |
| 8 |
| Amene amachitira chitsiru ulemu ali ngati munthu wokulunga mwala m'khwenengwe. |
| 9 |
| Monga imachitira minga yobaya dzanja la chidakwa ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru. |
| 10 |
| Amene amalemba ntchito chitsiru chongodziyendera kapena chidakwa, ali ngati munthu woponya mivi amene amangolasa anthu chilaselase. |
| 11 |
| Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake chili ngati galu wodya masanzi ake omwe. |
| 12 |
| Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa. |
| 13 |
| Waulesi amati, “Pali mkango pa njira! Mumseumo muli mkango!” |
| 14 |
| Monga chitseko chimatembenukira uku ndi uku pa zomangira zake, ndimonso waulesi amangokunkhulira pabedi pake. |
| 15 |
| Waulesi amati akapisa dzanja lake m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake. |
| 16 |
| Waulesi amadziyesa wanzeru kupambana anthu asanu ndi aŵiri amene angathe kuyankha mochenjera. |
| 17 |
| Amene angoloŵerera ndeu ya eniake, ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera. |
| 18 |
| Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa, |
| 19 |
| ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!” |
| 20 |
| Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu. |
| 21 |
| Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano. |
| 22 |
| Mau a kazitape ali ngati zakudya zokoma, zimene zimatsikira m'mimba msanga. |
| 23 |
| Monga m'mene chiziro chimakutira chiŵiya chadothi, ndimonso mau oshashalika amabisira mtima woipa. |
| 24 |
| Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga. |
| 25 |
| Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa. |
| 26 |
| Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu. |
| 27 |
| Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha, amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo. |
| 28 |
| Munthu wonama amadana ndi amene iye adaŵapweteka, pakamwa poshashalika mpoononga. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/026.mp3
31
26