|
| 1 |
|
| Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, Adzasweka modzidzimuka, palibe comciritsa. |
|
| 2 |
|
| Pocuruka olungama anthu akondwa; Koma polamulira woipa anthu ausa moyo. |
|
| 3 |
|
| Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wace; Koma wotsagana ndi akazi adama amwaza cuma. |
|
| 4 |
|
| Mfumu akhazikitsa dziko ndi ciweruzo; Koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa. |
|
| 5 |
|
| Wosyasyalika mnzace Acherera mapazi ace ukonde. |
|
| 6 |
|
| M'kulakwa kwa woipa muli msampha; Koma wolungama ayimba, nakondwera. |
|
| 7 |
|
| Wolungama asamalira mlandu wa osauka; Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa. |
|
| 8 |
|
| Anthu onyoza atentha mudzi; Koma anzeru alezetsa mkwiyo. |
|
| 9 |
|
| Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, Ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere. |
|
| 10 |
|
| Anthu ankhanza ada wangwiro; Koma oongoka mtima asamalira moyowace. |
|
| 11 |
|
| Citsiru cibvumbulutsa mkwiyo wace wonse; Koma wanzeru auletsa nautontholetsa. |
|
| 12 |
|
| Mkuru akamvera cinyengo, Atumuki ace onse ali oipa, |
|
| 13 |
|
| Waumphawi ndi wotsendereza akumana; Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo. |
|
| 14 |
|
| Mfumu yolamulira osauka mwantheradi, Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse. |
|
| 15 |
|
| Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru; Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi. |
|
| 16 |
|
| Pocuruka oipa zolakwa zicuruka; Koma olungama adzaona kugwa kwao. |
|
| 17 |
|
| Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; Nadzasangalatsa moyo wako. |
|
| 18 |
|
| Popanda cibvumbulutso anthu amasauka; Koma wosunga cilamulo adalitsika. |
|
| 19 |
|
| Kapolo sangalangizidwe ndi mau, Pakuti azindikira koma osabvomera. |
|
| 20 |
|
| Kodi uona munthu wansontho m'mau ace? Ngakhale citsiru cidzacenjera, koma ameneyo ai. |
|
| 21 |
|
| Yemwe alera kapolo wace mwa ufulu kuyambira ubwana wace, Pambuyo pace adzadziyesa mwana wobala. |
|
| 22 |
|
| Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; Waukali acuruka zolakwa. |
|
| 23 |
|
| Kudzikuza kwa munthu kudzamcepetsa; Koma wokhala ndi mtima wodzicepetsa adzalemekezedwa. |
|
| 24 |
|
| Woyenda ndi mbala ada moyo wace wace; Amva kulumbira, koma osaulula kanthu. |
|
| 25 |
|
| Kuopa anthu kuchera msampha; Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka, |
|
| 26 |
|
| Ambiri afunafuna ciyanjano ca mkuru; Koma ciweruzo ca munthu cicokera kwa Yehova. |
|
| 27 |
|
| Munthu woipa anyansa olungama; Ndipo woongoka m'njira anyansa wocimwa. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/proverbs/029.mp3
31
29