|
| 1 |
|
| Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa. |
|
| 2 |
|
| Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo. |
|
| 3 |
|
| Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma. |
|
| 4 |
|
| Mfumu akhazikitsa dziko ndi chiweruzo; koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa. |
|
| 5 |
|
| Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde. |
|
| 6 |
|
| M'kulakwa kwa woipa muli msampha; koma wolungama aimba, nakondwera. |
|
| 7 |
|
| Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa. |
|
| 8 |
|
| Anthu onyoza atentha mudzi; koma anzeru alezetsa mkwiyo. |
|
| 9 |
|
| Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere. |
|
| 10 |
|
| Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake. |
|
| 11 |
|
| Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa. |
|
| 12 |
|
| Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa. |
|
| 13 |
|
| Waumphawi ndi wotsendereza akumana; Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo. |
|
| 14 |
|
| Mfumu yolamulira osauka mwantheradi, mpando wake udzakhazikika kufikira nthawi zonse. |
|
| 15 |
|
| Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi. |
|
| 16 |
|
| Pochuluka oipa zolakwa zichuluka; koma olungama adzaona kugwa kwao. |
|
| 17 |
|
| Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako. |
|
| 18 |
|
| Popanda chivumbulutso anthu amasauka; koma wosunga chilamulo adalitsika. |
|
| 19 |
|
| Kapolo sangalangizidwe ndi mau, pakuti azindikira koma osavomera. |
|
| 20 |
|
| Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai. |
|
| 21 |
|
| Yemwe alera kapolo wake mwa ufulu kuyambira ubwana wake, pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala. |
|
| 22 |
|
| Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa. |
|
| 23 |
|
| Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa. |
|
| 24 |
|
| Woyenda ndi mbala ada moyo wakewake; amva kulumbira, koma osawulula kanthu. |
|
| 25 |
|
| Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka. |
|
| 26 |
|
| Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova. |
|
| 27 |
|
| Munthu woipa anyansa olungama; ndipo woongoka m'njira anyansa wochimwa. |
|
|
|
|