|
| 1 |
|
| Mwana wanga, usayiwale malangizo anga, mtima wako usunge malamulo anga. |
|
| 2 |
|
| Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere. |
|
| 3 |
|
| Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako. |
|
| 4 |
|
| Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu. |
|
| 5 |
|
| Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. |
|
| 6 |
|
| Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako. |
|
| 7 |
|
| Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa. |
|
| 8 |
|
| Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba. |
|
| 9 |
|
| Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova. |
|
| 10 |
|
| Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo. |
|
| 11 |
|
| Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake. |
|
| 12 |
|
| Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye. |
|
| 13 |
|
| Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, |
|
| 14 |
|
| pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide. |
|
| 15 |
|
| Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru. |
|
| 16 |
|
| Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu. |
|
| 17 |
|
| Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere. |
|
| 18 |
|
| Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri. |
|
| 19 |
|
| Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba. |
|
| 20 |
|
| Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka ndiponso mitambo inagwetsa mvula. |
|
| 21 |
|
| Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino. Zimenezi zisakuchokere. |
|
| 22 |
|
| Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi. |
|
| 23 |
|
| Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu, ndipo phazi lako silidzapunthwa; |
|
| 24 |
|
| pamene ugona pansi, sudzachita mantha; ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma. |
|
| 25 |
|
| Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa, |
|
| 26 |
|
| pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha. |
|
| 27 |
|
| Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi. |
|
| 28 |
|
| Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano. |
|
| 29 |
|
| Usamukonzere chiwembu mnansi wako, amene anakhala nawe pafupi mokudalira. |
|
| 30 |
|
| Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa pamene iye sanakuchitire zoyipa. |
|
| 31 |
|
| Usachite naye nsanje munthu wachiwawa kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse. |
|
| 32 |
|
| Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama. |
|
| 33 |
|
| Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa, koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama. |
|
| 34 |
|
| Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa. |
|
| 35 |
|
| Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | | 34 | | 35 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/003.mp3
31
3