|
| 1 |
|
| Mau a Lemueli mfumu, uthenga umene amace anamphunzitsa. |
|
| 2 |
|
| Ciani mwananga, Ciani mwana wa mimba yanga? Ciani mwana wa zowinda zanga? |
|
| 3 |
|
| Musapereke mphamvu yako kwa akazi, Ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu. |
|
| 4 |
|
| Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo; Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti? |
|
| 5 |
|
| Kuti angamwe, naiwale malamulo, Naweruze mokhota anthu onse osautsidwa. |
|
| 6 |
|
| Wofuna kufa umpatse cakumwa caukali, Ndi vinyo kwa owawa mtima; |
|
| 7 |
|
| Amwe, narwale umphawi wace, Osakumbukiranso bvuto lace. |
|
| 8 |
|
| Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, Ndi mlandu wa amasiye onse. |
|
| 9 |
|
| Tsegula pakamwa pako, Nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi. |
|
| 10 |
|
| Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wace uposa ngale. |
|
| 11 |
|
| Mtima wa mwamuna wace umkhulupirira, Sadzasowa phindu. |
|
| 12 |
|
| Mkaziyo amcitira zabwino, si zoipa, Masiku onse a moyo wace. |
|
| 13 |
|
| Afuna ubweya ndi thonje, Nacita mofunitsa ndi manja ace. |
|
| 14 |
|
| Akunga zombo za malonda; Nakatenga zakudya zace kutari. |
|
| 15 |
|
| Aukanso kusanace, Napatsa banja lace zakudya, nagawira adzakazi ace nchito. |
|
| 16 |
|
| Asinkhasinkha za munda, naugula; Naoka mipesa ndi zipatso za manja ace. |
|
| 17 |
|
| Amanga m'cuuno mwace ndi mphamvu, Nalimbitsa mikono yace, |
|
| 18 |
|
| Azindikira kuti malonda ace ampindulira; Nyali yace sizima usiku. |
|
| 19 |
|
| Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lace, Nafumbata mtengo wace. |
|
| 20 |
|
| Aolowera cikhato cace osauka; Natambasulira aumphawi manja ace. |
|
| 21 |
|
| Saopera banja lace cipale cofewa; Pakuti banja lace lonse libvala mlangali. |
|
| 22 |
|
| Adzipangira zimbwi zamaangamaanga; Nabvala bafuta ndi guta woti biriwiri. |
|
| 23 |
|
| Mwamuna wace adziwika kubwalo, Pokhala pakati pa akuru a dziko. |
|
| 24 |
|
| Asoka maraya abafuta, nawagulitsa; Napereka mipango kwa wogulitsa malonda. |
|
| 25 |
|
| Abvala mphamvu ndi ulemu; Nangoseka nthawi ya m'tsogolo. |
|
| 26 |
|
| Atsegula pakamwa pace ndi nzeru, Ndipo cilangizo ca cifundo ciri pa lilime lace. |
|
| 27 |
|
| Ayang'anira mayendedwe a banja lace, Sadya zakudya za ulesi. |
|
| 28 |
|
| Anace adzanyamuka, nadzamucha wodala; Mwamuna wace namtama, nati, |
|
| 29 |
|
| Ana akazi ambiri anacita mwangwiro, Koma iwe uposa onsewo. |
|
| 30 |
|
| Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe; Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. |
|
| 31 |
|
| Mumpatse zipatso za manja ace; Ndi nchito zace zimtame kubwalo. |
|
|
|
|