|
| 1 |
|
| Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa. |
|
| 2 |
|
| Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga? Chiyani mwana wa zowinda zanga? |
|
| 3 |
|
| Musapereke mphamvu yako kwa akazi, ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu. |
|
| 4 |
|
| Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti? |
|
| 5 |
|
| Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa. |
|
| 6 |
|
| Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali, ndi vinyo kwa owawa mtima; |
|
| 7 |
|
| amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake. |
|
| 8 |
|
| Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse. |
|
| 9 |
|
| Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi. |
|
| 10 |
|
| Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. |
|
| 11 |
|
| Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu. |
|
| 12 |
|
| Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake. |
|
| 13 |
|
| Afuna ubweya ndi thonje, nachita mofunitsa ndi manja ake. |
|
| 14 |
|
| Akunga zombo za malonda; nakatenga zakudya zake kutali. |
|
| 15 |
|
| Aukanso kusanake, napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito. |
|
| 16 |
|
| Asinkhasinkha za munda, naugula; naoka mipesa ndi zipatso za manja ake. |
|
| 17 |
|
| Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake. |
|
| 18 |
|
| Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku. |
|
| 19 |
|
| Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake. |
|
| 20 |
|
| Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake. |
|
| 21 |
|
| Saopera banja lake chipale chofewa; pakuti banja lake lonse livala mlangali. |
|
| 22 |
|
| Adzipangira zimbwi zamawangamawanga; navala bafuta ndi guta wofiirira. |
|
| 23 |
|
| Mwamuna wake adziwika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko. |
|
| 24 |
|
| Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa ogulitsa malonda. |
|
| 25 |
|
| Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo. |
|
| 26 |
|
| Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake. |
|
| 27 |
|
| Ayang'anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. |
|
| 28 |
|
| Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, |
|
| 29 |
|
| Ana akazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo. |
|
| 30 |
|
| Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. |
|
| 31 |
|
| Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo. |
|
|
|
|