Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mwananga, mvera nzeru yanga; Cherera makutu ku luntha langa; |
| 2 |
| Ukasunge zolingalira, Milomo yako ilabadire zomwe udziwa. |
| 3 |
| Pakuti milomo ya mkazi waciwerewere ikukha uci; M'kamwa mwace muti see koposa mafuta. |
| 4 |
| Cimariziro cace ncowawa ngati civumulo, Ndi cakuthwa ngati lupanga lakuthwa konse konse. |
| 5 |
| Mayendedwe ace atsikira kuimfa; Mapazi ace aumirira kumanda; |
| 6 |
| Sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo; Mayendedwe ace adzandira dzandi dzandi osadziwa iye. |
| 7 |
| Ndipo tsopano ana, mundimvere, Musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga. |
| 8 |
| Siyanitsa njira yako kutari kwa iyeyo, Osayandikira ku khomo la nyumba yace; |
| 9 |
| Kuti ungapereke ulemu wako kwa ena, Ndi zaka zako kwa ankhanza; |
| 10 |
| Kuti mphamvu yako isakhutitse alendo, Ndi kuti usagwire nchito m'nyumba ya wacilendo; |
| 11 |
| Ungalire pa cimariziro cako, Pothera nyama yako ndi thupi lako; |
| 12 |
| Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo, Mtima wanga ndi kunyoza cidzudzulo; |
| 13 |
| Ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga; Ngakhale kucherera makutu kwa akundilanga mwambo! |
| 14 |
| Ndikadakhala m'zoipa zonse, M'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu. |
| 15 |
| Imwa madzi a m'citsime mwako, Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako. |
| 16 |
| Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja, Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala? |
| 17 |
| Ikhale ya iwe wekha, Si ya alendo okhala nawe ai. |
| 18 |
| Adalitsike kasupe wako; Ukondwere ndi mkazi wokula nayo. |
| 19 |
| Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo, Maere ace akukwanire nthawi zonse; Ukodwe ndi cikondi cace osaleka. |
| 20 |
| Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere, Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo? |
| 21 |
| Pakuti njira za munthu ziri pamaso pa Yehova, Asinkhasinkha za mayendedwe ace onse. |
| 22 |
| Zoipazacezacezidzagwira woipa; Adzamangidwa ndi zingwe za ucimo wace. |
| 23 |
| Adzafa posowa mwambo; Adzasocera popusa kwambiri. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/proverbs/005.mp3
31
5