Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi, tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa, |
| 2 |
| kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo. |
| 3 |
| Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta, |
| 4 |
| koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu; ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse. |
| 5 |
| Mapazi ake amatsikira ku imfa; akamayenda ndiye kuti akupita ku manda. |
| 6 |
| Iye saganizirapo za njira ya moyo; njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi. |
| 7 |
| Tsopano ana inu, mundimvere; musawasiye mawu anga. |
| 8 |
| Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo, usayandikire khomo la nyumba yake, |
| 9 |
| kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena; ndi zaka zako kwa anthu ankhanza, |
| 10 |
| kapenanso alendo angadyerere chuma chako ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena. |
| 11 |
| Potsiriza pa moyo wako udzabuwula, thupi lako lonse litatheratu. |
| 12 |
| Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo! Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo! |
| 13 |
| Sindinamvere aphunzitsi anga kapena alangizi anga. |
| 14 |
| Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke pakati pa msonkhano wonse.” |
| 15 |
| Imwa madzi a mʼchitsime chakochako, madzi abwino ochokera mʼchitsime chako. |
| 16 |
| Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu? Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda? |
| 17 |
| Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha, osati uyigawireko alendo. |
| 18 |
| Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako. |
| 19 |
| Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse. |
| 20 |
| Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo? |
| 21 |
| Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona, ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse. |
| 22 |
| Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha; zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha. |
| 23 |
| Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo, adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/005.mp3
31
5