|
| 1 |
|
| Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole, ngati walonjeza kumulipirira mlendo, |
|
| 2 |
|
| ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena, wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako. |
|
| 3 |
|
| Tsono popeza iwe mwana wanga wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse: pita msanga ukamupemphe mnansi wako; kuti akumasule! |
|
| 4 |
|
| Usagone tulo, usawodzere. |
|
| 5 |
|
| Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje, ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka. |
|
| 6 |
|
| Pita kwa nyerere, mlesi iwe; kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu! |
|
| 7 |
|
| Zilibe mfumu, zilibe woyangʼanira kapena wolamulira, |
|
| 8 |
|
| komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola. |
|
| 9 |
|
| Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe? Kodi tulo tako tidzatha liti? |
|
| 10 |
|
| Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule, |
|
| 11 |
|
| umphawi udzakugwira ngati mbala ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba. |
|
| 12 |
|
| Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa, |
|
| 13 |
|
| amatsinzinira maso ake, namakwakwaza mapazi ake ndi kulozaloza ndi zala zake, |
|
| 14 |
|
| amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu. |
|
| 15 |
|
| Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa. |
|
| 16 |
|
| Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: |
|
| 17 |
|
| maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa, |
|
| 18 |
|
| mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa, |
|
| 19 |
|
| mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale. |
|
| 20 |
|
| Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako. |
|
| 21 |
|
| Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako. |
|
| 22 |
|
| Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula. |
|
| 23 |
|
| Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni, |
|
| 24 |
|
| kukupulumutsa kwa mkazi wadama, zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere. |
|
| 25 |
|
| Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake, |
|
| 26 |
|
| paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse. |
|
| 27 |
|
| Kodi munthu angathe kutenga moto zovala zake osapsa? |
|
| 28 |
|
| Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto mapazi ake osapserera? |
|
| 29 |
|
| Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina. Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa. |
|
| 30 |
|
| Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala. |
|
| 31 |
|
| Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake. |
|
| 32 |
|
| Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru. Wochita zimenezi amangodziwononga yekha. |
|
| 33 |
|
| Adzalandira mabala ndi mʼnyozo, ndipo manyazi ake sadzamuchokera. |
|
| 34 |
|
| Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa, ndipo sadzachita chifundo pobwezera. |
|
| 35 |
|
| Iye savomera dipo lililonse; sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | | 34 | | 35 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/006.mp3
31
6