|
| 1 |
|
| Mwananga, sunga mau anga, Ukundike malangizo anga; |
|
| 2 |
|
| Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; Ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako. |
|
| 3 |
|
| Uwamange pa zala zako, Uwalembe pamtima pako; |
|
| 4 |
|
| Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga; Nuche luntha mbale wako. |
|
| 5 |
|
| Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere, Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace. |
|
| 6 |
|
| Pakuti pa zenera la nyumba yanga Ndinapenyera pa made ace; Ndinaona pakati pa acibwana, |
|
| 7 |
|
| Ndinazindikira pakati pa ang'ono Mnyamata wopanda nzeru, |
|
| 8 |
|
| Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace; |
|
| 9 |
|
| Pa madzulo kuli sisiro, Pakati pa usiku pali mdima, |
|
| 10 |
|
| Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira, Atabvala zadama wocenjera mtima, |
|
| 11 |
|
| Ali wolongolola ndi wosaweruzika, Mapazi ace samakhala m'nyumba mwace. |
|
| 12 |
|
| Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, Nabisalira pa mphambano zonse. |
|
| 13 |
|
| Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona; Nati kwa iye ndi nkhope yacipongwe, |
|
| 14 |
|
| Nsembe za mtendere ziri nane; Lero ndacita zowinda zanga. |
|
| 15 |
|
| Cifukwa cace ndaturuka kudzakucingamira, Kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza. |
|
| 16 |
|
| Ndayala zopfunda pakama panga, Nsaru zamangamanga za thonje la ku Aigupto, |
|
| 17 |
|
| Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira A mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere. |
|
| 18 |
|
| Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa; Tidzisangalatse ndi ciyanjano. |
|
| 19 |
|
| Pakuti mwamuna kulibe kwathu, Wapita ulendo wa kutari; |
|
| 20 |
|
| Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace, Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu. |
|
| 21 |
|
| Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace, Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace. |
|
| 22 |
|
| Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru; |
|
| 23 |
|
| Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace; Amtsata monga mbalame yotamangira msampha; Osadziwa kuti adzaononga moyo wace. |
|
| 24 |
|
| Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, Labadirani mau a m'kamwa mwanga. |
|
| 25 |
|
| Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo, Usasocere m'mayendedwe ace. |
|
| 26 |
|
| Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; Ndipo ophedwa ndi iye acurukadi. |
|
| 27 |
|
| Nyumba yace ndiyo njira ya kumanda, Yotsikira ku zipinda za imfa. |
|
|
|
|