Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa. |
| 2 |
| Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako. |
| 3 |
| Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako. |
| 4 |
| Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.” |
| 5 |
| Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo. |
| 6 |
| Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera. |
| 7 |
| Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru. |
| 8 |
| Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo. |
| 9 |
| Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima. |
| 10 |
| Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga. |
| 11 |
| (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve, iye ndi wosakhazikika pa khomo. |
| 12 |
| Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika, ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse). |
| 13 |
| Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti, |
| 14 |
| “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga. |
| 15 |
| Choncho ndinabwera kudzakumana nawe; ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza! |
| 16 |
| Pa bedi panga ndayalapo nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto. |
| 17 |
| Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni. |
| 18 |
| Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa; tiye tisangalatsane mwachikondi! |
| 19 |
| Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako; wapita ulendo wautali: |
| 20 |
| Anatenga thumba la ndalama ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.” |
| 21 |
| Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika. |
| 22 |
| Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha, |
| 23 |
| mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka. |
| 24 |
| Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena. |
| 25 |
| Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake. |
| 26 |
| Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu. |
| 27 |
| Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/007.mp3
31
7