|
| 1 |
|
| Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake? |
|
| 2 |
|
| Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu. |
|
| 3 |
|
| Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti, |
|
| 4 |
|
| Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse. |
|
| 5 |
|
| Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu. |
|
| 6 |
|
| Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama. |
|
| 7 |
|
| Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa. |
|
| 8 |
|
| Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka. |
|
| 9 |
|
| Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza. |
|
| 10 |
|
| Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino. |
|
| 11 |
|
| Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru. |
|
| 12 |
|
| Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino. |
|
| 13 |
|
| Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga. |
|
| 14 |
|
| Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu. |
|
| 15 |
|
| Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama. |
|
| 16 |
|
| Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko. |
|
| 17 |
|
| Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza. |
|
| 18 |
|
| Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika. |
|
| 19 |
|
| Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri. |
|
| 20 |
|
| Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo. |
|
| 21 |
|
| Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma. |
|
| 22 |
|
| “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine. |
|
| 23 |
|
| Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe. |
|
| 24 |
|
| Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa. |
|
| 25 |
|
| Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale, |
|
| 26 |
|
| lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi. |
|
| 27 |
|
| Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama, |
|
| 28 |
|
| pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama, |
|
| 29 |
|
| pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi. |
|
| 30 |
|
| Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake. |
|
| 31 |
|
| Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.” |
|
| 32 |
|
| “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga. |
|
| 33 |
|
| Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga. |
|
| 34 |
|
| Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa. |
|
| 35 |
|
| Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima. |
|
| 36 |
|
| Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.” |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | | 33 | | 34 | | 35 | | 36 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/008.mp3
31
8