|
| 1 |
|
| Kodi suja nzeru imaitana? Suja nzeru zomvetsera zinthu zimakweza mau ake? |
|
| 2 |
|
| Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira, imakaima pa mphambano za miseu. |
|
| 3 |
|
| Imafuula pafupi ndi zipata kumaso kwa mzinda, ndiponso pamakomo poloŵera, imati, |
|
| 4 |
|
| “Inu anthu, ndikukuitanani, kuitanaku ndikuitana anthu nonsenu. |
|
| 5 |
|
| Inu osadziŵa kanthunu, phunzirani nzeru, inu opusanu, khalani tcheru. |
|
| 6 |
|
| Mverani, ndikuuzani zazikulu kwambiri, pakamwa panga palankhula zolungama. |
|
| 7 |
|
| Pakamwa panga palankhula zoona, kulankhula zoipa nchinthu chonyansa m'kamwa mwanga. |
|
| 8 |
|
| Mau onse a pakamwa panga ngokondweretsa Mulungu, m'mau angawo mulibe zopotoka kapena zokhotakhota. |
|
| 9 |
|
| Mau anga ngoona kwa munthu womvetsa, ngokhoza kwa anthu odziŵa zinthu. |
|
| 10 |
|
| Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. |
|
| 11 |
|
| Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru. |
|
| 12 |
|
| Ine nzeru ndimakhalira limodzi ndi kuchenjera. Ndimadziŵa zinthu ndipo ndimaganiza moyenera. |
|
| 13 |
|
| Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo. |
|
| 14 |
|
| Ndili ndi uphungu ndi maganizo abwino. Ndimamvetsa bwino zinthu, ndilinso ndi mphamvu. |
|
| 15 |
|
| Ndimathandiza mafumu polamulira ndine, olamulira ndimaŵathandiza ndine kulamula zolungama. |
|
| 16 |
|
| Ndine ndimathandiza akalonga polamula, ndine ndimathandiza akuluakulu poweruza m'dziko. |
|
| 17 |
|
| Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza. |
|
| 18 |
|
| Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira. |
|
| 19 |
|
| Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi. |
|
| 20 |
|
| Ndimachita zomwe zili zoyenera, sindipatuka kuchoka m'njira za chilungamo. |
|
| 21 |
|
| Ndimaŵapatsa chuma anthu ondikonda, ndi kudzaza nyumba zao zosungiramo chuma. |
|
| 22 |
|
| “Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambirira ndinali ine. |
|
| 23 |
|
| Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe. |
|
| 24 |
|
| Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale. |
|
| 25 |
|
| Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo; |
|
| 26 |
|
| lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi. |
|
| 27 |
|
| Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire a nyanja yozama, |
|
| 28 |
|
| pamene ankaika thambo m'malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m'nyanja yozama, |
|
| 29 |
|
| pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi. |
|
| 30 |
|
| Nthaŵiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthaŵi zonse. |
|
| 31 |
|
| Ndinkasangalala m'dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu. |
|
| 32 |
|
| “Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. |
|
| 33 |
|
| Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga. |
|
| 34 |
|
| Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa. |
|
| 35 |
|
| Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta. |
|
| 36 |
|
| Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo. Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.” |
|
|
|
|