Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri. |
| 2 |
| Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake. |
| 3 |
| Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti, |
| 4 |
| “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti, |
| 5 |
| “Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza. |
| 6 |
| Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.” |
| 7 |
| Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake. |
| 8 |
| Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda. |
| 9 |
| Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake. |
| 10 |
| Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu. |
| 11 |
| Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa. |
| 12 |
| Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha. |
| 13 |
| Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu. |
| 14 |
| Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda, |
| 15 |
| kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo. |
| 16 |
| Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati, |
| 17 |
| “Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!” |
| 18 |
| Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/proverbs/009.mp3
31
9