Buku Loyera
|
| 1 |
| Nzeru idamanga nyumba yake, idaimika nsanamira zake zisanu ndi ziŵiri. |
| 2 |
| Idapha ziŵeto zake, idakonza vinyo wake, nkuyala tebulo lake. |
| 3 |
| Idatuma adzakazi ake kuti akakhalire pa malo apamwamba mu mzinda ndipo akalengeze kuti, |
| 4 |
| “Munthu wamba aliyense abwere kuno!” Kwa munthu wopanda nzeru imati, |
| 5 |
| “Bwera, dzadyeko chakudya changa, ndipo udzamweko vinyo amene ndakonza. |
| 6 |
| Leka kupulukira kwako, kuti ukhale ndi moyo, uziyenda m'njira ya nzeru.” |
| 7 |
| Woyesa kukonza munthu wonyoza, amangonyozekerapo, wodzudzula munthu woipa, amangopwetekerapo. |
| 8 |
| Wonyoza usamdzudzule, angadane nawe. Koma ukadzudzula munthu wanzeru, adzakukonda. |
| 9 |
| Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa. |
| 10 |
| Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu. |
| 11 |
| Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako. |
| 12 |
| Ngati ndiwe wanzeru, phindu ndi lako. Ngati umanyoza ena, udzavutika ndiwe wekha. |
| 13 |
| Mkazi wopusa ngwaphokoso, ngwosachangamuka, ndiponso wosamvetsa zinthu. |
| 14 |
| Amakhala pakhomo pa nyumba yake, pamalo pena pooneka bwino mu mzinda. |
| 15 |
| Akatero nkumaitana amene akudutsapo, amene akungodziyendera, osafuna kupatuka. |
| 16 |
| “Amati, inu anthu wamba, tapatukirani muno!” Tsono kwa wopanda nzeru amati, |
| 17 |
| “Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.” |
| 18 |
| Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/proverbs/009.mp3
31
9