|
| 1 |
|
| Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu. |
|
| 2 |
|
| Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere. |
|
| 3 |
|
| Inde, poyendanso chitsiru panjira, nzeru yake imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine chitsiru. |
|
| 4 |
|
| Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri. |
|
| 5 |
|
| Pali choipa ndachiona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkulu; |
|
| 6 |
|
| utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi. |
|
| 7 |
|
| Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akopolo. |
|
| 8 |
|
| Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma. |
|
| 9 |
|
| Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema. |
|
| 10 |
|
| Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza. |
|
| 11 |
|
| Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho. |
|
| 12 |
|
| Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza. |
|
| 13 |
|
| Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa. |
|
| 14 |
|
| Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake? |
|
| 15 |
|
| Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumudzi. |
|
| 16 |
|
| Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa! |
|
| 17 |
|
| Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai. |
|
| 18 |
|
| Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ake; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja. |
|
| 19 |
|
| Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse. |
|
| 20 |
|
| Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo. |
|
|
|
|