Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndine duwa lofiira la ku Saroni, ngakhale kakombo wa kuzigwa. |
| 2 |
| Ngati kakombo pakati pa minga momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi. |
| 3 |
| Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga. |
| 4 |
| Anandifikitsa kunyumba ya vinyo, mbendera yake yondizolimira inali chikondi. |
| 5 |
| Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula, pakuti ndadwala ndi chikondi. |
| 6 |
| Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu, dzanja lake lamanja ndi kundifungatira. |
| 7 |
| Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala za kuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini. |
| 8 |
| Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza, alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda. |
| 9 |
| Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pakhoma lathu. Apenyera pazenera, nasuzumira pamade. |
| 10 |
| Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine, tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye. |
| 11 |
| Pakuti, taona, chisanu chatha, mvula yapita yaleka; |
| 12 |
| maluwa aoneka pansi; nthawi yoimba mbalame yafika, mau a njiwa namveka m'dziko lathu. |
| 13 |
| Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima, mipesa niphuka, inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu. |
| 14 |
| Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka, ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako; pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola. |
| 15 |
| Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono, amene akuononga minda yamipesa; pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri. |
| 16 |
| Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake: aweta zake pakati akakombo. |
| 17 |
| Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/songofsolomon/002.mp3
8
2