Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ine ndine duwa la ku Saroni, duwa lokongola la ku zigwa. |
| 2 |
| Monga duwa lokongola pakati pa minga ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana. |
| 3 |
| Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga. |
| 4 |
| Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi. |
| 5 |
| Undidyetse keke ya mphesa zowuma, unditsitsimutse ndi ma apulosi, pakuti chikondi chandifowoketsa. |
| 6 |
| Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira. |
| 7 |
| Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. |
| 8 |
| Tamverani bwenzi langa! Taonani! Uyu akubwera apayu, akulumphalumpha pa mapiri, akujowajowa pa zitunda. |
| 9 |
| Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera. |
| 10 |
| Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine, “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, ndipo tiye tizipita. |
| 11 |
| Ona, nyengo yozizira yatha; mvula yatha ndipo yapitiratu. |
| 12 |
| Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu. |
| 13 |
| Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira; mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga tiye tizipita.” |
| 14 |
| Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe, mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri, onetsa nkhope yako, nʼtamvako liwu lako; pakuti liwu lako ndi lokoma, ndipo nkhope yako ndi yokongola. |
| 15 |
| Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa. |
| 16 |
| Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake; amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola. |
| 17 |
| Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/songofsolomon/002.mp3
8
2