Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola; maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zooneka pa phiri la Giliyadi. |
| 2 |
| Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga, zokwera kuchokera kosamba; yonse ili ndi ana awiri, palibe imodzi yopoloza. |
| 3 |
| Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseli pa chophimba chako. |
| 4 |
| Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida, apachikapo zikopa zikwi, ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu. |
| 5 |
| Mawere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi, akudya pakati pa akakombo. |
| 6 |
| Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, ndikamuka kuphiri la mure, ndi kuchitunda cha lubani. |
| 7 |
| Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe, mulibe chilema mwa iwe. |
| 8 |
| Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi, kuchokera nane ku Lebanoni: Unguza pamwamba pa Amana, pa nsonga ya Seniri ndi Heremoni, pa ngaka za mikango, pa mapiri a anyalugwe. |
| 9 |
| Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako. |
| 10 |
| Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu! |
| 11 |
| M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni. |
| 12 |
| Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza. |
| 13 |
| Mphukira zako ndi munda wamakangaza, ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido. |
| 14 |
| Narido ndi chikasu, nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani; mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka. |
| 15 |
| Ndiwe kasupe wa m'minda, chitsime cha madzi amoyo, ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni. |
| 16 |
| Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwera; nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo. Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake, nadye zipatso zake zofunika. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/songofsolomon/004.mp3
8
4