Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi. |
| 2 |
| Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene, zochokera kozisambitsa kumene. Iliyonse ili ndi ana amapasa; palibe imene ili yokha. |
| 3 |
| Milomo yako ili ngati mbota yofiira; pakamwa pako ndi pokongola kwambiri. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza. |
| 4 |
| Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo. |
| 5 |
| Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala, ngati ana amapasa a nswala amene akudya pakati pa maluwa okongola. |
| 6 |
| Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, ndidzapita ku phiri la mure ndi ku chitunda cha lubani. |
| 7 |
| Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe. |
| 8 |
| Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga, tiye tichoke ku Lebanoni, utsikepo pa msonga ya Amana, kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni, kuchoka ku mapanga a mikango ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa. |
| 9 |
| Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako. |
| 10 |
| Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse! |
| 11 |
| Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni. |
| 12 |
| Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa; ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa. |
| 13 |
| Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza; muli zipatso zokoma kwambiri, muli hena ndi nadi, |
| 14 |
| nadi ndi safiro, kalamusi ndi sinamoni, komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino. Mulinso mure ndi aloe ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri. |
| 15 |
| Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda, chitsime cha madzi oyenda, mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni. |
| 16 |
| Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/songofsolomon/004.mp3
8
4