Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga; ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga. Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani abwenzi anga, imwani; Inu okondana, imwani kwambiri. |
| 2 |
| Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso. Tamverani, bwenzi langa akugogoda: “Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.” |
| 3 |
| Ndavula kale zovala zanga, kodi ndizivalenso? Ndasamba kale mapazi anga kodi ndiwadetsenso? |
| 4 |
| Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko; mtima wanga unagunda chifukwa cha iye. |
| 5 |
| Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo, ndipo manja anga anali noninoni ndi mure, zala zanga zinali mure chuchuchu, pa zogwirira za chotsekera. |
| 6 |
| Ndinamutsekulira wachikondi wanga, koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita. Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake. Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze. Ndinamuyitana koma sanandiyankhe. |
| 7 |
| Alonda anandipeza pamene ankayendera mzindawo. Anandimenya ndipo anandipweteka; iwo anandilanda mwinjiro wanga, alonda a pa khoma aja! |
| 8 |
| Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani, mukapeza wokondedwa wangayo, kodi mudzamuwuza chiyani? Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi. |
| 9 |
| Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji? Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani kuti uzichita kutipempha motere? |
| 10 |
| Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi pakati pa anthu 1,000. |
| 11 |
| Mutu wake ndi golide woyengeka bwino; tsitsi lake ndi lopotanapotana, ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala. |
| 12 |
| Maso ake ali ngati nkhunda mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, ngati nkhunda zitasamba mu mkaka, zitayima ngati miyala yamtengowapatali. |
| 13 |
| Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati maluwa okongola amene akuchucha mure. |
| 14 |
| Manja ake ali ngati ndodo zagolide zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali. Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu woyikamo miyala ya safiro. |
| 15 |
| Miyendo yake ili ngati mizati yamwala, yokhazikika pa maziko a golide. Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni, abwino kwambiri ngati mkungudza. |
| 16 |
| Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri; munthuyo ndi wokongola kwambiri! Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/songofsolomon/005.mp3
8
5