Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Bwenzi lako wapita kuti, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako wapatukira kuti, tikamfunefune pamodzi nawe? |
| 2 |
| Bwenzi langa watsikira kumunda kwake, kuzitipula za mphoka, kukadya kumunda kwake, ndi kutchera akakombo. |
| 3 |
| Ndine wake wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine; aweta zake pakati pa akakombo. |
| 4 |
| Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza, wokoma ngati Yerusalemu, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera. |
| 5 |
| Undipambutsire maso ako, pakuti andiopetsa. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zigona pambali pa Giliyadi. |
| 6 |
| Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi, zikwera kuchokera kosamba; yonse ili ndi ana awiri, palibe imodzi yopoloza. |
| 7 |
| Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseli pa chophimba chako. |
| 8 |
| Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi, kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ndi anamwali osawerengeka. |
| 9 |
| Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana akazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda. |
| 10 |
| Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera? |
| 11 |
| Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa. |
| 12 |
| Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimika pakati pa magaleta a anthu anga aufulu. |
| 13 |
| Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe; bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe. Muyang'aniranji pa Msulami, ngati pa masewero akuguba? |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/songofsolomon/006.mp3
8
6