Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti kuti timufunefune pamodzi ndi iwe? |
| 2 |
| Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake, ku timinda ta zokometsera zakudya, akukadyetsa ziweto zake ku minda, ndiponso akuthyola maluwa okongola. |
| 3 |
| Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola. |
| 4 |
| Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza, wokongola kwambiri ngati Yerusalemu, ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera. |
| 5 |
| Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi. |
| 6 |
| Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa, iliyonse ili ndi ana amapasa, palibe imene ili yokha. |
| 7 |
| Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu, masaya ako ali ngati mabandu a makangadza. |
| 8 |
| Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60, ndi azikazi 80, ndi anamwali osawerengeka; |
| 9 |
| koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda. |
| 10 |
| Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha, wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja? |
| 11 |
| Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa. |
| 12 |
| Ndisanazindikire kanthu, ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga. |
| 13 |
| Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami; bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe! Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami, pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri? |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/songofsolomon/006.mp3
8
6