Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga, woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; osandinyoza munthu. |
| 2 |
| Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, kuti andilange mwambo; ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, ndi madzi a makangaza anga. |
| 3 |
| Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu, lamanja lake ndi kundifungatira. |
| 4 |
| Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi, chisanafune mwini. |
| 5 |
| Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe. |
| 6 |
| Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova. |
| 7 |
| Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu. |
| 8 |
| Tili ndi mlongwathu wamng'ono, alibe mawere; timchitirenji mlongo wathu tsiku lokhoma unkhoswe wake? |
| 9 |
| Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva: Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza. |
| 10 |
| Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere. |
| 11 |
| Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni; nabwereka alimi mundawo; yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake. |
| 12 |
| Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu; nacho chikwicho, Solomoni iwe, koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri. |
| 13 |
| Namwaliwe wokhala m'minda, anzako amvera mau ako: Nanenanso undimvetse. |
| 14 |
| Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga, dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mphoka. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/songofsolomon/008.mp3
8
8