Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga, amene anayamwa mawere a amayi anga! Ndikanakumana nawe pa njira, ndikanakupsompsona, ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza. |
| 2 |
| Ndikanakutenga ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, amayi amene anandiphunzitsa, ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, zotsekemera za makangadza. |
| 3 |
| Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira. |
| 4 |
| Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani: musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. |
| 5 |
| Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo. |
| 6 |
| Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu. |
| 7 |
| Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. |
| 8 |
| Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono, koma alibe mawere, kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu pa tsiku limene adzamufunsire? |
| 9 |
| Ngati iye ndi khoma, tidzamumangira nsanja ya siliva. Ngati iye ndi chitseko, tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza. |
| 10 |
| Ine ndili ngati khoma, ndipo mawere anga ndi nsanja zake. Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa ndine wobweretsa mtendere. |
| 11 |
| Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni; iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi, aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake. |
| 12 |
| Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000 ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo. |
| 13 |
| Iwe amene umakhala mʼminda uli pamodzi ndi anzako, ndilole kuti ndimve liwu lako! |
| 14 |
| Fulumira wokondedwa wanga, ndipo ukhale ngati gwape kapena mwana wa mbawala wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/songofsolomon/008.mp3
8
8