Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Katundu wa Moabu. Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe. |
| 2 |
| Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa. |
| 3 |
| M'makwalala mwao adzimangira ciguduli m'cuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri. |
| 4 |
| Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace. |
| 5 |
| Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko. |
| 6 |
| Pakuti pa madzi a Nimirimi padzakhala mabwinja; papeza udzu wafota, msipu watha. |
| 7 |
| Cifukwa cace zocuruka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo ku mtsinje wa mabango. |
| 8 |
| Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Moabu; kukuwa kwace kwafikira ku Eglaimu, ndi kukuwa kwace kwafikira ku Beerelimu. |
| 9 |
| Pakuti madzi a Dimoni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa! Dimoni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Moabu, ndi pa otsala am'dziko. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/isaiah/015.mp3
66
15