Buku Loyera
|
| 1 |
| Nawu ulosi wonena za chipululu cha m'mbali mwa nyanja. Tsoka lidzafika kuchokera ku dziko lochititsa mantha monga m'mene kamvulumvulu amakunthira kuchokera ku chipululu. |
| 2 |
| Ndaona zinthu zoopsa m'masomphenya: wofunkha akufunkha, woononga akuwononga. Ankhondo a ku Elamu, yambani nkhondo! Ankhondo a ku Mediya, zingani mzindawo. Ine Chauta ndidzathetsa mavuto onse amene adadza ndi Babiloni. |
| 3 |
| Nchifukwa chake zimene ndidazimva ndi kuziwona m'masomphenya zija zandichititsa mantha, ndipo ndamva nazo ululu ngati mkazi amene akuchira. Ndikuvutika nazo zimene ndilikumva. Ndikuda nazo nkhaŵa zimene ndikuwonazi. |
| 4 |
| Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha. Ndakhala ndikulakalaka chisisira, koma chisisiracho chandibweretsera zoopsa. |
| 5 |
| Iwo akukonza tebulo ndi kuyala mphasa, alikudya, alikumwa. Mwadzidzidzi alikumva mau akuti, Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu! |
| 6 |
| Pakuti Ambuye andiwuza kuti, “Pita, kaike mlonda kuti azinena zimene akuwona. |
| 7 |
| Akamaona anthu aŵiriaŵiri okwera pa akavalo, okwera pa abulu ndi okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru, tcherutu zedi!” |
| 8 |
| Apo mlondayo adafuula kuti, “Ambuye, usana wonse ndimakhala pa nsanja, usiku wonse ndimakhala pa malo anga olondera. |
| 9 |
| Ndidangoona kukubwera anthu okwera pa akavalo, akuyenda aŵiriaŵiri. Mmodzi mwa iwo adati, ‘Ii, wagwa, wagwatu uku Babiloni! Mafano onse a milungu yake aphwanyikira pansi.’ ” |
| 10 |
| Ndiye abale anga Aisraele, inu opunthidwa ndi opetedwa ngati tirigu, tsopano ndakuuzani uthenga umene ndamva kwa Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. |
| 11 |
| Nawu ulosi wonena za Edomu: Wina akundilankhula mofuula kuchokera ku Edomu, akuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?” |
| 12 |
| Mlonda akuti, “Kulikucha, koma kudanso. Ukafuna kufunsanso, ubwerenso udzafunse.” |
| 13 |
| Nawu ulosi wonena za Arabiya: Inu anthu a ku Dedani oyenda pa gulu, amene usiku mumagona m'malunje a ku Arabiya, |
| 14 |
| muŵapatse madzi anthu aludzu kuti amwe. Inu anthu a ku Tema, muŵapatse chakudya anthu othaŵa nkhondo. |
| 15 |
| Pakuti akuthaŵa malupanga, malupanga osololasolola, mauta okokakoka, ndiponso nkhondo yoopsa. |
| 16 |
| Ambuye adandiwuza kuti, “Chatsala chaka chimodzi, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ndipo ulemu wonse wa anthu a ku Kedara udzatheratu. |
| 17 |
| Mwa anthu onse amphamvu a ku Kedara okoka mauta, opulumuka adzakhala oŵerengeka.” Chauta, Mulungu wa Israele, watero. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/isaiah/021.mp3
66
21