×

Buku Loyera

YESAYA 22

1
Nawu ulosi wonena za chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya: Kodi chachitika nchiyani kuti nonse mukwere pa madenga?
2
Ndinu anthu osokera, okhala mu mzinda wachiwawa ndi waphokoso. Anthu anu ophedwa sadaphedwe ndi lupanga, kapena kufera pankhondo.
3
Atsogoleri anu onse adathaŵa nagwidwa, osaponyako ndi muvi umodzi womwe. Nonsenu amene mudapezeka mudagwidwa, ngakhale mudaathaŵiratu adani akali kutali.
4
Nchifukwa chake ndidati, “Muchoke, mundileke ndilire ndi mtima woŵaŵa. Musayese kundipepesa pa za kuwonongeka kwa abale anga.”
5
Nthaŵi ino ndi yamavuto, yogonjetsedwa ndiponso yachisokonezo m'chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ndiwo atichita zimenezi. Malinga adagumuka ndipo anthu adakalirira ku mapiri.
6
Ankhondo a ku Elamu adadza atakwera pa akavalo, m'manja muli mauta ndi mivi, ndipo ankhondo a ku Kiri anali okonzeka ndi zishango zao.
7
Zigwa zanu zachonde zinali zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo adakaima kumaso kwa zipata za mzinda.
8
Zonse zoteteza Yuda zidalandidwa. Tsiku limenelo mudayang'ana ku zida zankhondo zimene zinali m'Nyumba ya Nkhalango ija.
9
Mudapeza malo ena m'makoma a mzinda wa Yerusalemu ali ogumuka. Mudasunga madzi m'chidziŵe chakunsi.
10
Mudaŵerenga nyumba zonse mu mzinda wa Yerusalemu, ndipo mudagwetsa zina kuti mupeze miyala yokonzera makoma a mzindawo.
11
Pakati pa makoma aŵiri mudamangapo chitsime chosungiramo madzi ochokera ku chidziŵe chakale. Koma simudaganizeko za Mulungu amene adachititsa zimenezi, simudasamaleko za Iye amene adazikonza kale lomwe.
12
Nthaŵi imeneyo Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adakuitanani kuti mulire ndi kudza misozi, kumeta ndi kuvala ziguduli.
13
Koma inu mudakondwa ndi kusangalala, mudapha ng'ombe ndi nkhosa ndi kuzidya, ndiponso mudamwa vinyo. Mudati, “Tidye, timwe, poti maŵa tifa.”
14
Chauta Wamphamvuzonse adandiwululira pondinong'oneza m'khutu kuti, “Ndithudi, tchimo limeneli sindidzakukhululukirani mpaka kufa kwanu,” akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
15
Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adandiwuza kuti ndipite kwa Sebina, kapitao woyang'anira nyumba yaufumu, kukamufunsa kuti,
16
“Kodi ukuchita chiyani kuno? Walimba mtima bwanji kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri, ndi kudzisemera mopumulira m'thanthwe?
17
Chauta adzakugwira dzolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iweyo wanyongawe.
18
Adzakusandutsa ngati mpira ndipo adzakuponya m'dziko lalikulu. Kumeneko nkumene ukafere, ndipo magaleta ako amene unkanyadira adzatsalira komwekonso, iwe wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wakowe.
19
Chauta adzakuchotsa pa ukapitao wako, ndipo adzakutsitsa pakuthetsa udindo wako.”
20
Chauta adauza Sebina kuti, “Tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu, mwana wa Hilikiya.
21
Ndidzam'veka mkanjo wako ndi lamba wako ndi kumpatsa ulamuliro wako. Tsono adzalamulira anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.
22
Ndidzampatsa makii a ulamuliro wa pa banja la mfumu Davide. Akadzatsekula, palibe amene adzatseke. Ndipo adzatseka, popanda wina wotsekula.
23
Ndidzamulimbitsa ngati chikhomo pa udindo wakewo, ndipo adzakhala wopatsa ulemu kwa banja la atate ake.
24
“Koma ana ndi adzukulu ake adzakhala katundu wolemera pa iye m'banja la atate ake, monga ngati ziŵiya zonse zimene zimapachikidwa pa chikhomo.
25
Tsiku limenelo chikhomo chokhoma dzolimba chija chidzasukusa, chidzazuka ndipo chidzagwa. Tsono zonse zopachikidwa pachikhomopo zidzaonongedwa.” Akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba