×

Buku Lopatulika 1992

YESAYA 26

1
Tsiku limenelo adzayimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tiri ndi mudzi wolimba; Iye adzaikacipulumutso cikhale macemba ndi malinga.
2
Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene ucita zoonadi, ulowemo.
3
Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni weni, cifukwa ukukhulupirirani Inu.
4
Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lacikhalire.
5
Cifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa pfumbi.
6
Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.
7
Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
8
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.
9
Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.
10
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.
11
Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.
12
Yehova, udzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira nchito zathu zonse.
13
Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzachula dzina lanu.
14
Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; cifukwa cace Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa cikumbukiro cao conse.
15
Mwacurukitsa mtundu, Yehova, mwacurukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.
16
Yehova, iwo adza kwa Inu mobvutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.
17
Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.
18
Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.
19
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muyimbe, inu amene mukhala m'pfumbi; cifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzaturutsa mizimu.
20
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.
21
Pakuti taonani, Yehova adza kucokera ku malo ace kudzazonda okhala pa dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao; dziko lidzabvumbulutsa mwazi wace, ndipo silidzabvundikiranso ophedwa ace.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba