1
Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu! Tsoka kwa ulemerero wake umene wayamba kufota ngati duŵa, mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde, umene amanyadira anthu oledzera vinyo.
2
Ambuye ali naye wina wamphamvu ndi wanyonga. Iyeyo adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe woononga, ngati chigumula chamadzi chokokolola zonse, ndipo adzaŵagwetsa pansi mwankhanza.
3
Kunyada kwa atsogoleri oledzera a ku Efuremu adzakuthetseratu kwenikweni.
4
Ndipo ulemerero wa mzinda uja umene uli ngati duŵa lokhala kumtunda kwa chigwa chachonde wayamba kufota. Udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa. Munthu akangoiwona, amaithyola ndi kuidya nthaŵi yomweyo.
5
Tsiku limenelo Chauta Wamphamvuzonse adzakhala ngati chisoti chachifumu chaulemerero ndi nsangamutu yokongola kwa anthu ake otsala.
6
Oweruza adzaŵapatsa mtima wachilungamo. Adzaŵalimbitsa mtima onse amene amalimbana ndi adani pa zipata za mzinda.
7
Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira.
8
Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha, palibenso malo opanda uve.
9
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akuti aphunzitse yani? Kodi uthengawo akuti afotokozere yani? Kodi ndife ana ongoleka kumene kuyamwa, kapena makanda ongoŵachotsa kumene kubere?
10
Akuyesa kumatiphunzitsa pang'onopang'ono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezo akungoti apa pang'ono, apa pang'ono.”
11
Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo, anthu a chilankhulo chamtundu.
12
Adaakuuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo ousira ndi ano,” koma inu simudamvere.
13
Nchifukwa chake Chauta adzakuphunzitsani pang'onopang'ono, lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro, kuti mudzakhumudwe poyenda. Mudzapweteka, mudzakodwa mu msampha, ndipo adzakutengani ku ukapolo.
14
Tsopano mverani zimene Chauta akukuuzani, inu anthu achipongwe, amene mumalamulira anthu ake kuno ku Yerusalemu.
15
Inu mumanena kuti “Ife tidachita chipangano ndi imfa, ndipo manda satiwopsa ai. Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse. Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira, ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.”
16
Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti, “Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika, mwala wapangodya wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu. Pamwalapo palembedwa kuti, ‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’
17
Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe choyesera maziko ake, ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake. Koma matalala adzaononga mabodza amene mumaŵakhulupirira, ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.”
18
Chipangano chimene mudachita ndi imfa chidzatha, kotero kuti manda adzayamba kukuwopsani. Chiwonongeko chikamadzafika, chidzakugonjetsani.
19
Nthaŵi iliyonse imene chizidzaoneka, chizidzakukanthani. Chizidzafika m'maŵa mulimonse, usana ndi usiku. Tsono anthu akadzamvetsa uthenga umenewu, adzaopsedwa kwambiri.
20
Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri, kotero kuti sangatambalitsepo miyendo, ndiponso ngati munthu wofunda kabulangete kopereŵera.
21
Chauta adzamenya nkhondo monga adachitira ku phiri la Perazimu. Adzakalipa monga adachitira ku chigwa cha Gibiyoni. Adzachita zimene afuna, ngakhale kuti zidzaoneke ngati zachilendo. Adzatsiriza ntchito yake, ntchito yake yozizwitsayo.
22
Tsono inu musanyozere mau ameneŵa. Mukatero, maunyolo anu adzakuthinani koposa. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, andiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzaononga dziko lonse.”
23
Tcherani khutu, ndipo mumve mau anga. Mvetserani ndipo mumve zimene ndikukuuzani.
24
Kodi mlimi wofuna kubzala amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugaula ndi kugalauza?
25
Akasalaza mundawo, suja amafesa maŵere ndi chitoŵe? Suja amafesa tirigu ndi barele m'mizere, nabzala mcheŵere m'mphepete mwa mundawo?
26
Mulungu ndiye amamulangiza ndi kumphunzitsa njira yokhoza.
27
Maŵere sapuntha poponderezapo ndi gareta lopanda mikombero, ndipo chitoŵe sapuntha popondetsapo mikombero ya gareta. Maŵere amapuntha ndi kamtengo, chitoŵe amaomba ndi ndodo.
28
Tirigu sangamupunthe kosalekeza, kuwopa kuti angatekedzeke. Amampuntha poyendetsapo galeta, koma osatekedza njere zake.
29
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi