Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Aigupto kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magareta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israyeli, ngakhale kumfuna Yehova! |
| 2 |
| Koma Iyenso ali wanzeru, nadzatengera coipa, ndipo sadzabwezanso mau ace, koma adzaukira banja la ocita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira nchito yoipa. |
| 3 |
| Koma Aaigupto ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lace, wothandiza adzapunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera. |
| 4 |
| Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yace, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupitikitsa, ngakhale kudzicepetsa wokha, cifukwa ca phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo ku phiri la Ziyoni, ndi kucitunda kwace komwe. |
| 5 |
| Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wamakamu adzacinjiriza Yerusalemu; Iye adzacinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga. |
| 6 |
| Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israyeli inu. |
| 7 |
| Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ace asiliva, ndi mafano ace agolidi amene manja anu anu anawapanga akucimwitseni inu. |
| 8 |
| Pamenepo Asuri adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammariza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ace adzalamba. |
| 9 |
| Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/isaiah/031.mp3
66
31