×

Buku Loyera

YESAYA 32

1
Nthaŵi ina kudzakhala mfumu ina yolamulira mwaungwiro, ndiponso nduna zina zoweruza mwachilungamo.
2
Aliyense mwa iwo adzakhala ngati pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe. Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma, ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu.
3
Maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzakhala otchera.
4
Anthu a mtima waphamphu adzadziŵa kuchita zinthu moganiza bwino, ndipo anthu achibwibwi adzalankhula mosadodoma ndi momveka.
5
Chitsiru sichidzalandira ulemu, ndipo munthu woipa sadzalemekezeka.
6
Munthu wopusa amalankhula zauchitsilu, ndipo amaganiza kuchita zoipa. Amachita zoipira Mulungu, amalankhula zonyoza Mulungu. Anjala saŵapatsa chakudya, aludzu saŵapatsa chakumwa.
7
Munthu wachabechabe njira zake nzoipa. Amalingalira zaupandu kuti aŵachite chiwembu anthu osauka pakuŵanamizira, ngakhale pamene osaukawo ali osalakwa konse.
8
Koma munthu wa mtima wabwino amalingalira zabwino, ndipo amalimbikira kuchita zabwino.
9
Tatiyeni, inu akazi aulesi, mumve mau anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikulankhula.
10
Pakapita chaka ndi masiku pang'ono, mudzanjenjemera inu akazi amatama, chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika, zipatsonso sizidzaoneka.
11
Dederani inu akazi aulesi, njenjemerani, inu odzikhulupirira udyo. Vulani zovala, ndipo muvale nsanza m'chiwuno.
12
Dzimenyeni pa chifuŵa mwachisoni, chifukwa minda yachonde ndi yamphesa yaonongeka,
13
ndipo minga ndi mkandankhuku zikumera pa dziko la anthu anga. Ndithu, mulire nyumba zonse zimene ankakhalamo mosangalala, ndiponso mzinda umene udaali ndi chimwemwe.
14
Nyumba yaufumu idzasiyidwa, ndipo mzinda wonse udzakhala wopanda anthu. Malinga ake ndi nsanja yomwe zidzasanduka mapanga mpaka muyaya. Abulu akuthengo adzasangalala kumeneko, ndipo ziŵeto zidzapeza busa komweko.
15
Koma Mulungu adzatitumizira mzimu wake, kuchokera kumwamba, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka lachonde, minda yonse idzabereka dzinthu dzambiri.
16
Pamenepo m'dziko lonse mudzakhala chilungamo, kuyambira ku chipululu mpaka ku minda yachonde.
17
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
18
Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
19
Komabe nkhalango idzaonongedwa ndi matalala, ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi.
20
Anthu adzakondwa kwambiri chifukwa adzakhala ndi madzi ambiri, ndipo abulu ndi ng'ombe zao azidzadya paliponse.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba