×

Buku Loyera

YESAYA 47

1
Chauta akunena kuti, “Iwe namwali, Babiloni, tsika ndi kukhala pa fumbi. Iwe namwali, Kaldeya, khala pansi, opanda mpando waufumu. Pakuti sadzakutchulanso wofeŵa ndi wodzitekemeza.
2
Tenga mphero kuti upere ufa. Chotsa nsalu yako yakumaso. Kwinda zovala zako mpaka m'ntchafu, woloka mitsinje.
3
Maliseche ako adzakhala poyera, ndipo udzachita manyazi kwambiri. Ndidzalipsira, ndipo palibe amene adzandiletsa.”
4
Woyera uja wa Israele ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Chauta Mphambe.
5
Akuuza Babiloni kuti, “Khala chete ndi kuloŵa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya. Sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.
6
Ndidaŵakwiyira anthu anga, ndidaŵanyoza ngati si anthu anga. Ndidaŵapereka m'manja mwako, ndipo iwe sudaŵachitire chifundo. Udaumira mtima ndi nkhalamba zomwe.
7
Unkaganiza kuti nthaŵi zonse udzakhala mfumukazi, mwakuti zinthu zimenezi sudazisamale, sudaganizirenso m'mene zidzathere.”
8
“Nchifukwa chake tsono umvetsere izi, iwe wongokonda zokondweretsawe, iwe amene umakhala pabwino, numaganiza mumtima mwako kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai. Sindidzakhala konse wamasiye, ndipo ana anga sadzafa.’ ”
9
Koma m'kamphindi, tsiku limodzi, zinthu ziŵiri zonsezi zidzakugwera. Ana ako onse kukufera, iweyo kusanduka wamasiye, zonsezo zidzakugwera pamodzi, ngakhale kuti uli ndi matsenga ambiri ndi zithumwa zamphamvu.
10
“Sunkada nako nkhaŵa konse kuipa kwako, unkaganiza kuti palibe wokupenya. Kuchenjera kwako ndi nzeru zako zidakusokeza, ndipo mumtima mwako unkaganiza kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.’ ”
11
Tsoka lidzakugwera, ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako. Chiwonongeko chidzakufikira, iwe osatha kuchithaŵa, chipasupasu chosayembekezeka konse chidzakugwera mwadzidzidzi.
12
Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako.
13
Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira.
14
“Taona, anthuwo ali ngati mapesi, adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya malaŵi ake. Moto wake si woti nkuwotha kapena kusendera pafupi nawo ai.
15
Ndimo m'mene adzakuthandizire anthuwo amene wakhala ukugwira nao ntchito ndi kuchita nao malonda chiyambire cha ubwana wako. Onsewo adzangomwazikana, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba