×

Buku Loyera

YESAYA 48

1
Mverani izi inu a banja la Yakobe, inu amene dzina lanu amakutchulani Aisraele, inu zidzukulu za Yuda. Inu mumalumbira dzina la Chauta, ndipo mumapemphera kwa Mulungu wa Israele, pamene zimenezo sizichokera mu mtima woona ndi wolungama.
2
Komabe inu mukunyada kuti ndinu nzika za mzinda wopatulika ndipo kuti mumakhulupirira Mulungu wa Israele, amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
3
Chauta akuuza Israele kuti, “Zimene zidachitika poyamba ndidaaloseratu kalekale, zidaatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndidaazilengeza. Tsono mwadzidzidzi ndidachitapo kanthu, ndipo zidaonekadi.
4
Ndidaadziŵa kuti ndiwe wokanika, wa nkhongo gwa, ndi wa mutu wouma.
5
Ndidaakuuziratu zakutsogolo kalekale. Zisanachitike ndidaazilengezeratu kwa iwe, kuti usadzanene kuti, ‘Fano langa ndilo lidachita zimenezi, fano langa losema ndi fano langa loumba ndiwo adalamula kuti zichitike!’
6
“Zonsezi udazimva, tsono uzilingalire bwino. Monga iweyo sungazivomereze? Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno ndidzakuuza zinthu zatsopano, zinthu zobisika zimene sudazidziŵe konse.
7
Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale. Mpaka lero unali usanazimve konse, kuwopa kuti ungamati, ‘Zimenezi ndiye ai, ndidazidziŵa kale.’
8
Chikhalire sudamve chikhalire sudadziŵe, nkale lonse makutu ako sanali otsekuka. Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu, ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako adakutchula waupandu.
9
“Kuti anthu alemekeze dzina langa ndikuchedwetsa mkwiyo wanga. Kuti anthu aone ulemerero wanga ndikukulezera ukali wanga, kuti ndisakuwononge kotheratu.
10
Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva, ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso.
11
Chifukwa cha ulemu wanga, ulemu wanga wokha, ndiye ndimachita zonse. Ndingalole bwanji kuti dzina langa linyozeke? Ulemerero wanga sindidzapatsa wina ai.”
12
Chauta akunena kuti, “Mverani Ine, inu zidzukulu za Yakobe, inu Aisraele, amene ndidakuitanani. Mulungu uja ndine, ndine woyamba ndipo ndine wotsiriza.
13
Manja anga adamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja lidafunyulula mlengalenga. Ndikaitana dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, zonsezo zimabwera pamodzi kwa Ine.
14
“Sonkhanani nonsenu, ndipo mumvetsere. Mwa milungu ina ndani adalosapo zimenezi? Amene Chauta amamkonda uja adzachita zomwe Chautayo adakonzera Babiloni, ndi dzanja lake lamphamvu adzalimbana ndi Akaldeya.
15
Ndine amene ndidalankhula ndi kumuitana. Ndidambweretsa ndine, ndipo zonse zidzamuyendera bwino.
16
Bwerani pafupi tsono, kuti mumve zimene nditi ndinene. Kuyambira pa chiyambi sindidalankhule mobisa, nthaŵi imene zimenezo zinkachitika, nkuti Ine ndilipo.” Tsono Ambuye Chauta andipatsa Mzimu wao, ndipo andituma.
17
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
18
Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.
19
Ana ako akadachuluka ngati mchenga, ndipo zidzukulu zako ngati fumbi. Dzina lao silikadachotsedwa pamaso panga, silikadafafanizika konse.
20
“Tulukani m'dziko la Babiloni, thaŵani m'dziko la ukapolo. Mulengeze zimenezi ndi mau amphamvu, muzilalike, muzifikitse mpaka ku mathero a dziko lapansi. Muzinena kuti, ‘Chauta waombola Yakobe, mtumiki wake.’ ”
21
Pamene ankatsogolera anthu ake m'chipululu, iwo sadamve ludzu. Adaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe. Adang'amba thanthwelo, ndipo mudatuluka madzi.
22
“Koma anthu ochimwa alibe mtendere,” akuterotu Chauta.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba