×

Buku Loyera

YESAYA 64

1
Inu Chauta, bwanji osang'amba mlengalenga kuti mutsike pansi? Bwanji osati mapiri agwedezeke poona Inu,
2
monga momwe moto umatenthera tchire, ndiponso monga momwe umagadutsira madzi, kuti adani anu akudziŵeni, ndipo kuti anthu a mitundu ina anjenjemere pamaso panu.
3
Nthaŵi ina yake mudatsika pansi pano kudzachita zinthu zoopsa zimene sitidaziyembekeze. Mapiri atakuwonani, adanjenjemera ndi mantha.
4
Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe amene adaona kapena kumva za Mulungu wina wonga Inu, wochitira zotere anthu omkhulupirira.
5
Inu mumaŵalandira onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amayesetsa kuyenda monga Inu mufunira. Inde mudatikwiyira, komabe ife tidapitiriza kuchimwa. Takhala ochimwadi nthaŵi yaitali, kodi tidzapulumuka kumene?
6
Tonsefe tasanduka ngati anthu oipitsidwa, ndipo ntchito zathu zonse zabwino zakhala ngati nsanza zauve. Tonsefe tikufota ngati masamba, tikuuluzika ndi machimo athu, ngati tikuuluzika ndi mphepo.
7
Palibe amene amatamira dzina lanu popemphera, kapena amene amatekeseka nzopempha chithandizo kwa Inu. Mwatifulatira ndipo mwatisandutsa akapolo a machimo athu.
8
Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu.
9
Motero musatikwiyire kopitirira, ndipo musakumbukire machimo athu mpaka muyaya. Tapota nanu mutiganizireko, tonsefetu ndife anthu anu.
10
Mizinda yanu yoyera yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka thengo, Yerusalemu wasanduka wamasiye.
11
Nyumba yathu yoyera ndi yokongola, m'mene makolo athu ankakutamandirani, yapsa ndi moto. Malo onse amene tinkaŵakonda asanduka bwinja.
12
Kodi Inu Chauta, simukuvutika nazo zimenezi? Monga mudzangokhala chete nkumatizunza mwankhanza?
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba