Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo Pasuri mwana wace wa Imeri wansembe, amene anali kapitao wamkuru m'nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya alikunenera zimenezi. |
| 2 |
| Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali m'cipata ca kumtunda ca Benjamini, cimene cinali ku nyumba ya Yehova. |
| 3 |
| Ndipo panali m'mawa mwace, kuti Pasuri anaturutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanacha dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu. |
| 4 |
| Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe coopsa ca kwa iwe mwini, ndi kwa abale ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babulo, nadzawapha ndi lupanga, |
| 5 |
| Ndiponso ndidzapereka cuma conse ca mudzi uwu, ndi zaphindu zace zonse, ndi zinthu zace zonse za mtengo wace, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babulo. |
| 6 |
| Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babulo, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza. |
| 7 |
| Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala coseketsa dzuwa lonse, lonse andiseka. |
| 8 |
| Pakuti pali ponse ndinena, ndipfuula; ndipfuula, Ciwawa ndi cofunkha; pakuti mau a Mulungu ayesedwa kwa ine citonzo, ndi coseketsa, dzuwa lonse. |
| 9 |
| Ndipo ngati nditi, Sindidzamchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lace, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso. |
| 10 |
| Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera cilango. |
| 11 |
| Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsya; cifukwa cace ondisautsa adzapunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, cifukwa sanacita canzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika. |
| 12 |
| Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona imso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera cilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga. |
| 13 |
| Muyimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ocita zoipa. |
| 14 |
| Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine. |
| 15 |
| Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye. |
| 16 |
| Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mpfuu mamawa, ndi mkuwo pausana; |
| 17 |
| cifukwa sanandipha ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yace yaikuru nthawi zonse. |
| 18 |
| Cifukwa canji ndinaturuka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi? |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/jeremiah/020.mp3
52
20