Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa. |
| 2 |
| Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira. |
| 3 |
| Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga. |
| 4 |
| Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu. |
| 5 |
| Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga. |
| 6 |
| Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu. |
| 7 |
| Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo woononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo. |
| 8 |
| Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerera pa ife. |
| 9 |
| Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa. |
| 10 |
| Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo. |
| 11 |
| Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa; |
| 12 |
| mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo. |
| 13 |
| Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka. |
| 14 |
| Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati? |
| 15 |
| Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efuremu: |
| 16 |
| Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera midzi ya Yuda mau ao. |
| 17 |
| Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova. |
| 18 |
| Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako. |
| 19 |
| Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo. |
| 20 |
| Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi. |
| 21 |
| Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga? |
| 22 |
| Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa. |
| 23 |
| Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika. |
| 24 |
| Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka. |
| 25 |
| Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa. |
| 26 |
| Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo midzi yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa. |
| 27 |
| Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa. |
| 28 |
| Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo. |
| 29 |
| Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo. |
| 30 |
| Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako. |
| 31 |
| Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/jeremiah/004.mp3
52
4