Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli, bwererani kwa Ine,” akutero Yehova. “Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga ndipo musasocherenso. |
| 2 |
| Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’ Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse ndipo adzanditamanda.” |
| 3 |
| Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi: “Limani masala anu musadzale pakati pa minga. |
| 4 |
| Dziperekeni nokha kwa Ine kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse, inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani, chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo popanda wina wowuzimitsa. |
| 5 |
| “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’ |
| 6 |
| Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni! Musachedwe, thawani kuti mupulumuke! Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko choopsa.” |
| 7 |
| Monga mkango umatulukira mʼngaka yake momwemonso wowononga mayiko wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake. Watero kuti awononge dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda wokhalamo. |
| 8 |
| Choncho valani ziguduli, lirani ndi kubuwula, pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova sunatichokere. |
| 9 |
| “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima, ansembe adzachita mantha kwambiri, ndipo aneneri adzathedwa nzeru,” akutero Yehova. |
| 10 |
| Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.” |
| 11 |
| Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; |
| 12 |
| koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.” |
| 13 |
| Taonani, adani akubwera ngati mitambo, magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu, akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga. Tsoka ilo! Tawonongeka! |
| 14 |
| Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti? |
| 15 |
| Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani; akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu. |
| 16 |
| Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina, lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti, ‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda. |
| 17 |
| Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda, chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ” akutero Yehova. |
| 18 |
| “Makhalidwe anu ndi zochita zanu zakubweretserani zimenezi. Chimenechi ndiye chilango chanu. Nʼchowawa kwambiri! Nʼcholasa mpaka mu mtima!” |
| 19 |
| Mayo, mayo, ndikumva kupweteka! Aa, mtima wanga ukupweteka, ukugunda kuti thi, thi, thi. Sindingathe kukhala chete. Pakuti ndamva kulira kwa lipenga; ndamva mfuwu wankhondo. |
| 20 |
| Tsoka limatsata tsoka linzake; dziko lonse lasanduka bwinja. Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa, mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa. |
| 21 |
| Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo, ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti? |
| 22 |
| Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.” |
| 23 |
| Ndinayangʼana dziko lapansi, ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu; ndinayangʼana thambo, koma linalibe kuwala kulikonse. |
| 24 |
| Ndinayangʼana mapiri, ndipo ankagwedezeka; magomo onse ankangosunthira uku ndi uku. |
| 25 |
| Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu; mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa. |
| 26 |
| Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu; mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake. |
| 27 |
| Yehova akuti, “Dziko lonse lidzasanduka chipululu komabe sindidzaliwononga kotheratu. |
| 28 |
| Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira ndipo thambo lidzachita mdima, pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima, ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.” |
| 29 |
| Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi, anthu a mʼmizinda adzathawa. Ena adzabisala ku nkhalango; ena adzakwera mʼmatanthwe mizinda yonse nʼkuyisiya; popanda munthu wokhalamo. |
| 30 |
| Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja! Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira ndi kuvalanso zokometsera zagolide? Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera, ukungodzivuta chabe. Zibwenzi zako zikukunyoza; zikufuna kuchotsa moyo wako. |
| 31 |
| Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka, kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba. Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu. Atambalitsa manja awo nʼkumati, “Kalanga ife! Tikukomoka. Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/jeremiah/004.mp3
52
4