Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Uwu ndi uthenga umene mneneri Yeremiya anawuza Baruki mwana wa Neriya mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa mwana ya Yosiya kuti alembe mʼbuku. |
| 2 |
| “Yehova Mulungu wa Israeli, akunena kwa iwe Baruki kuti: |
| 3 |
| Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ” |
| 4 |
| Koma Yehova akukuwuza kuti, “Ndidzagwetsa chimene ndinamanga ndipo ndidzazula chimene ndinadzala. Ndidzachita zimenezi mʼdziko lonse. |
| 5 |
| Kodi tsono ukudzifunira wekha zinthu zazikulu? Usadzifunire. Pakuti ndidzagwetsa mavuto pa anthu onse, koma ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungadzapite.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/jeremiah/045.mp3
52
45