Buku Loyera
|
| 1 |
| Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya, onena za Afilisti, Farao asanaononge Gaza. |
| 2 |
| Adati, “Onani m'mene madzi akubwerera kuchokera kumpoto, adzakhala mtsinje wosefukira ndi wamkokomo. Adzasefukira m'dzikomo ndi kumiza zonse zokhala m'menemo, mizinda yonse, ndi anthu onse okhalamo. Anthu azidzafuula, onse okhala m'dzikomo azidzalira. |
| 3 |
| Adzamva mgugu wa akavalo othamanga, adzamva phokoso la magaleta ake, ndi kulira kwa mikombero yake. Atate sadzaganizirako za ana ao, adzangokhala ali manja lende! |
| 4 |
| Ndithu tsiku lidzafika limene Afilisti onse adzaonongeka, tsiku limene adzaphedwe otsala onse amene ati adzathandize mzinda wa Tiro ndi Sidoni. Pakuti Chauta adzaononga Afilisti, onse otsala a ku chilumba cha Krete. |
| 5 |
| A ku Gaza adzameta mipala yachisoni, A ku Asikeloni adzangoti chete. Inu otsala mwa Afilisti, kodi ndi mpaka liti mudzakhale mukudzichekacheka chifukwa cha kulira? |
| 6 |
| Mukuti, ‘Ha, Chauta lupanga lili m'manja! Kodi adzapumula liti? Aliloŵetse m'chimake, likhale momwemo, lipumule.’ |
| 7 |
| Kodi lupangalo lingapumule bwanji pamene Chauta walipatsa kale ntchito yoti limchitire? Walituma kuti likalimbane ndi Asikeloni, kuti likathire nkhondo anthu a m'mbali mwa nyanja.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/jeremiah/047.mp3
52
47