Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, |
| 2 |
| Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova. |
| 3 |
| Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano. |
| 4 |
| Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa. |
| 5 |
| Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; |
| 6 |
| ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo; |
| 7 |
| ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya. |
| 8 |
| Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa. |
| 9 |
| Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa, |
| 10 |
| ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi? |
| 11 |
| Kodi nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova. |
| 12 |
| Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele. |
| 13 |
| Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha; |
| 14 |
| chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo. |
| 15 |
| Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu. |
| 16 |
| Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe. |
| 17 |
| Kodi suona iwe chimene achichita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu? |
| 18 |
| Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga. |
| 19 |
| Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao? |
| 20 |
| Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima. |
| 21 |
| Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama. |
| 22 |
| Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera; |
| 23 |
| koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni. |
| 24 |
| Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo. |
| 25 |
| Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo; |
| 26 |
| koma sanandimvere Ine sanatchera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao. |
| 27 |
| Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe. |
| 28 |
| Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao. |
| 29 |
| Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira. |
| 30 |
| Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti alipitse. |
| 31 |
| Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa m'mtima mwanga. |
| 32 |
| Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa. |
| 33 |
| Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa. |
| 34 |
| Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/jeremiah/007.mp3
52
7