Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, |
| 2 |
| Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uli wonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango? |
| 3 |
| Kodi atengako mtengo kupanga nao nchito? atengako ciciri kodi kupacikapo cipangizo ciri conse? |
| 4 |
| Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zace zonse ziwiri, nupserera pakati pace, kodi ukomera nchito Irf yonse? |
| 5 |
| Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera nchito iri yonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso nchito iri yonse? |
| 6 |
| Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu. |
| 7 |
| Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzaturuka kumoto, koma moto udzawatha; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse. |
| 8 |
| Ndipo ndidzasandutsa dziko cipululu; popeza anacita colakwa, ati Ambuye Yehova. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/ezekiel/015.mp3
48
15